Kodi ma webusaiti ndi Matsamba a Nchezo zatsekedwa? Netiweki yanu ikuchedwa modabwitsa? Gwilitsani OONI Probe kuti mudziwe!

Ndi OONI, mutha kufufuza kutsekedwa kwa mawebusaiti ndi njila zotumizilana uthenga pompopompo, kupima liwilo ndi machitidwe a netiweki, komanso kudziwa ngati netiweki  yanu ili ndi kuthekela kukhetha ndi chidiso.

OONI Probe yapangidwa ndi a Open Observatory of Network Interference (OONI), imene ndi ntchito yokonza software yaulele (pansi pa Tor Project)  ndicholinga chobweletsa poyela mchitidwe wokhetha intaneti padziko lapansi.

Kuyamba mu 2012, OONI’s padziko lonse yatolela mazana a mpimo wa netiweki kuchokela mmaiko oposa 200 , kuonetsa nkhani zochuluka za kusokoneza mwadala netiweki. 

Sonkhetsani umboni wa makhetha pa intaneti
Mutha kufufuza pamene komanso mmene mawebusaiti ndi njila zapelekela uthenga pompompo zatsekedwa.  Zotsatila mudzapeze mukapima netiweki zidzatha kutengedwa ngati umboni wa makhetha pa intaneti. 

Zizindikileni njila zothandizila makhetha ndi chidiso
Mpima wa OONI Probe umapangidwa kutinso ufukule kepezeka kwa njila (middleboxes) zochitila makhetha ndi chidiso.

Pimani liwilo ndi mchitidwe a netiweki yanu
Mutha kupima liwilo ndi mchitidwe wa netiweki yanu pogwilitsa ntchito Network Diagnostic Test (NDT) ya OONI. Muthanso kupima mmene kuonela kanema kuchitila pogwilitsa ntchito  Adaptive Streaming over HTTP (DASH).

Uthenga opezeka
OONI imasindikiza uthenga opeseka pa kupima netiweki chifukwa uthenga wa aliyense umalola ena kutha kutsimikizila zotsatilazi, kuchita kafukufuku wapadela, komanso kuyankha mafunso ena a kafukuku. Kusindikiza poyela kwa zotsatila za OONI kumabweletsa poyela makhetha a intaneti padziko lonse . Pezani zambili za OONI apa: https://ooni.io/data/

Sofitiweya yaulere
Zonse zimene OONI Probe imakgwilitsa ntchito pakupima  (kuphatikizapo NDT komanso DASH), zigwilitsa ntchito sofitiweya yaulele komanso nditopezekela aliyense. mungathe kupeza sofitiweya ya OONI pa GitHub: https://github.com/ooni. Mukufuna kudziwa zambili zammene OONI Probe amagwilila ntchito? Pezani zambili pa: https://ooni.io/nettest/

Kuti mulandile nkhani ndi zina zofunikila zatsopano kuchokela ku OONI-verse, tsatilani tsamba lathu la Twitter: https://twitter.com/OpenObservatory
